Salimo 124
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 1 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, 
anene tsono Israeli, 
 2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, 
potiwukira anthuwo, 
 3 iwo atatipsera mtima, 
akanatimeza amoyo; 
 4 chigumula chikanatimiza, 
mtsinje ukanatikokolola, 
 5 madzi a mkokomo 
akanatikokolola. 
 6 Atamandike Yehova, 
amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. 
 7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame 
yokodwa mu msampha wa mlenje; 
msampha wathyoka, 
ndipo ife tapulumuka. 
 8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova 
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.