Salimo 122
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 1 Ndinakondwera atandiwuza kuti, 
“Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” 
 2 Mapazi athu akuyima mʼzipata 
zako, Iwe Yerusalemu. 
 3 Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda 
umene uli wothithikana pamodzi. 
 4 Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, 
mafuko a Yehova, 
umboni wa kwa Israeli, 
kuti atamande dzina la Yehova. 
 5 Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, 
mipando yaufumu ya nyumba ya Davide. 
 6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: 
“Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino. 
 7 Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, 
ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.” 
 8 Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga 
ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.” 
 9 Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, 
ndidzakufunira zabwino.