Masalimo  
BUKU LOYAMBA 
 1
Masalimo 1–41 
 1 Wodala munthu 
amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, 
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, 
kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza. 
 2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova 
ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku. 
 3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, 
umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake 
ndipo masamba ake safota. 
Chilichonse chimene amachita amapindula nacho. 
 4 Sizitero ndi anthu oyipa! 
Iwo ali ngati mungu 
umene umawuluzidwa ndi mphepo. 
 5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo, 
kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama. 
 6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, 
koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.