Nahumu  
 1
 1 Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi. 
Mkwiyo wa Yehova pa Ninive 
 2 Yehova ndi Mulungu wansanje 
ndiponso wobwezera; 
Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. 
Yehova amabwezera adani ake 
ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo. 
 3 Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; 
ndipo sadzalola kuti munthu 
wolakwa asalangidwe. 
Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, 
ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake. 
 4 Amalamulira nyanja ndipo imawuma; 
amawumitsa mitsinje yonse. 
Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma 
ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota. 
 5 Mapiri amagwedera pamaso pake 
ndipo zitunda zimasungunuka. 
Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, 
dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo. 
 6 Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? 
Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? 
Ukali wake ukuyaka ngati moto; 
matanthwe akunyeka pamaso pake. 
 7 Yehova ndi wabwino, 
ndiye kothawirako nthawi ya masautso. 
Amasamalira amene amamudalira, 
 8 koma ndi madzi achigumula choopsa 
Iye adzawononga adani ake (Ninive); 
adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima. 
 9 Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova 
adzachiwononga kotheratu; 
msautso sudzabweranso kachiwiri. 
 10 Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga 
ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; 
adzatenthedwa ngati ziputu zowuma. 
 11 Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, 
wofuna kuchitira Yehova chiwembu, 
amene amapereka uphungu woyipa. 
 12 Yehova akuti, 
“Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, 
kaya iwowo ndi ambiri, 
koma adzawonongedwa ndi kutheratu. 
Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, 
sindidzakuzunzanso. 
 13 Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako 
ndipo ndidzadula maunyolo ako.” 
 14 Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, 
“Sudzakhala ndi zidzukulu 
zimene zidzadziwike ndi dzina lako. 
Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba 
amene ali mʼnyumba ya milungu yako. 
Ine ndidzakukumbira manda 
chifukwa ndiwe woyipitsitsa.” 
 15 Taonani, pa phiripo, 
mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, 
amene akulengeza za mtendere! 
Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu 
ndipo kwaniritsani malumbiro anu. 
Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; 
iwo adzawonongedwa kotheratu.