Salimo 150
 1 Tamandani Yehova. 
Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; 
mutamandeni ku thambo lake lamphamvu. 
 2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; 
mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. 
 3 Mutamandeni poyimba malipenga, 
mutamandeni ndi pangwe ndi zeze. 
 4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, 
mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro. 
 5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, 
mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri. 
 6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. 
Tamandani Yehova.