Salimo 129
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 
 1 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” 
anene tsono Israeli; 
 2 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, 
koma sanandipambane. 
 3 Anthu otipula analima pa msana panga 
ndipo anapangapo mizere yayitali: 
 4 Koma Yehova ndi wolungama; 
Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” 
 5 Onse amene amadana ndi Ziyoni 
abwezedwe pambuyo mwamanyazi. 
 6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, 
umene umafota usanakule; 
 7 sungadzaze manja a owumweta 
kapena manja a omanga mitolo. 
 8 Odutsa pafupi asanene kuti, 
“Dalitso la Yehova lili pa inu; 
tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”