Salimo 112
 1 Tamandani Yehova. 
Wodala munthu amene amaopa Yehova, 
amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake. 
 2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko; 
mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa. 
 3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, 
ndipo chilungamo chake ndi chosatha. 
 4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima; 
wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima. 
 5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, 
amene amachita ntchito yake mwachilungamo. 
 6 Ndithu sadzagwedezeka; 
munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya. 
 7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; 
mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova. 
 8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha; 
potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano. 
 9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, 
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya; 
nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu. 
 10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; 
adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. 
Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.