Salimo 101
Salimo la Davide. 
 1 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; 
kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando. 
 2 Ndidzatsata njira yolungama; 
nanga mudzabwera liti kwa ine? 
Ndidzayenda mʼnyumba mwanga 
ndi mtima wosalakwa. 
 3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa 
pamaso panga. 
Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; 
iwo sadzadziphatika kwa ine. 
 4 Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; 
ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine. 
 5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri 
ameneyo ndidzamuletsa; 
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, 
ameneyo sindidzamulekerera. 
 6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, 
kuti akhale pamodzi ndi ine; 
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa 
adzanditumikira. 
 7 Aliyense wochita chinyengo 
sadzakhala mʼnyumba mwanga. 
Aliyense woyankhula mwachinyengo 
sadzayima pamaso panga. 
 8 Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu 
onse oyipa mʼdziko; 
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa 
mu mzinda wa Yehova.