Salimo 96
 1 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; 
Imbirani Yehova dziko lonse lapansi. 
 2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; 
lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. 
 3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, 
ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. 
 4 Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; 
ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse. 
 5 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, 
koma Yehova analenga mayiko akumwamba. 
 6 Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, 
mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika. 
 7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, 
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu. 
 8 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; 
bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake. 
 9 Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; 
njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi. 
 10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” 
Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; 
Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama. 
 11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; 
nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; 
 12 minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo. 
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe; 
 13 idzayimba pamaso pa Yehova, 
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; 
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo 
ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.