Salimo 93
 1 Yehova akulamulira, wavala ulemerero; 
Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu, 
dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe. 
 2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale; 
Inu ndinu wamuyaya. 
 3 Nyanja zakweza Inu Yehova, 
nyanja zakweza mawu ake; 
nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo. 
 4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri, 
ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja, 
Yehova mmwamba ndi wamphamvu. 
 5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika; 
chiyero chimakongoletsa nyumba yanu 
mpaka muyaya.