Salimo 53
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide. 
 1 Chitsiru chimati mu mtima mwake, 
“Kulibe Mulungu.” 
Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; 
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino. 
 2 Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano 
pa ana a anthu 
kuti aone ngati alipo wina wanzeru, 
wofunafuna Mulungu. 
 3 Aliyense wabwerera, 
iwo onse pamodzi akhala oyipa; 
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino, 
ngakhale mmodzi. 
 4 Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; 
anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, 
ndipo sapemphera kwa Mulungu? 
 5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu 
pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. 
Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; 
inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza. 
 6 Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! 
Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, 
lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!