Salimo 43
 1 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; 
ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; 
mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa. 
 2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. 
Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? 
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, 
woponderezedwa ndi mdani? 
 3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu 
kuti zinditsogolere; 
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, 
kumalo kumene inu mumakhala. 
 4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, 
kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. 
Ndidzakutamandani ndi zeze, 
Inu Mulungu wanga. 
 5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga? 
Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? 
Khulupirira Mulungu, 
pakuti ndidzamutamandabe Iye, 
Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.