Salimo 30
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. 
 1 Ndidzakukwezani Yehova, 
chifukwa mwanditulutsa kwakuya, 
ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine. 
 2 Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo 
ndipo Inu munandichiritsa. 
 3 Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, 
munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. 
 4 Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; 
tamandani dzina lake loyera. 
 5 Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi 
koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; 
utha kuchezera kulira usiku wonse, 
koma chimwemwe chimabwera mmawa. 
 6 Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, 
“Sindidzagwedezekanso.” 
 7 Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, 
munachititsa phiri langa kuyima chilili; 
koma pamene munabisa nkhope yanu, 
ndinataya mtima. 
 8 Kwa Inu Yehova ndinayitana; 
kwa Ambuye ndinapempha chifundo; 
 9 “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga 
ngati nditsikira ku dzenje? 
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? 
Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu? 
 10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; 
Yehova mukhale thandizo langa.” 
 11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; 
munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe, 
 12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. 
Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.