Salimo 28
Salimo la Davide. 
 1 Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; 
musakhale osamva kwa ine. 
Pakuti mukapitirira kukhala chete, 
ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. 
 2 Imvani kupempha chifundo kwanga 
pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, 
pomwe ndikukweza manja anga 
kuloza ku malo anu oyeretsetsa. 
 3 Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, 
pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, 
amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo 
koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo. 
 4 Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo 
ndi ntchito zawo zoyipa; 
abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita 
ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera. 
 5 Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova, 
ndi zimene manja ake anazichita, 
Iye adzawakhadzula 
ndipo sadzawathandizanso. 
 6 Matamando apite kwa Yehova, 
popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga. 
 7 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; 
mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. 
Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe 
ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo. 
 8 Yehova ndi mphamvu ya anthu ake, 
linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake. 
 9 Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu; 
mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya.