Salimo 14
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. 
 1 Chitsiru chimati mu mtima mwake, 
“Kulibe Mulungu.” 
Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; 
palibe amene amachita zabwino. 
 2 Yehova kumwamba wayangʼana pansi, 
kuyangʼana anthu onse 
kuti aone ngati alipo wina wanzeru, 
amene amafunafuna Mulungu. 
 3 Onse atembenukira kumbali, 
onse pamodzi asanduka oyipa; 
palibe amene amachita zabwino, 
palibiretu ndi mmodzi yemwe. 
 4 Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? 
Akudya anthu anga ngati chakudya chawo 
ndipo satamanda Yehova? 
 5 Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, 
pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama. 
 6 Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka, 
koma Yehova ndiye pothawirapo pawo. 
 7 Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! 
Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, 
Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!