32
Mawu a Elihu 
 1 Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.  2 Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.  3 Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.  4 Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.  5 Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima. 
 6 Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: 
“Ine ndine wamngʼono, 
inuyo ndinu akuluakulu, 
nʼchifukwa chake ndimaopa, 
ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa. 
 7 Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; 
anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’ 
 8 Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, 
mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu. 
 9 Si okalamba amene ali ndi nzeru, 
si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera. 
 10 “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; 
inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’ 
 11 Ndadikira nthawi yonseyi, 
ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, 
pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule, 
 12 ineyo ndinakumvetseranidi. 
Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; 
palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake. 
 13 Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; 
Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’ 
 14 Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, 
ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira. 
 15 “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; 
mawu awathera. 
 16 Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, 
pakuti angoyima phee wopanda yankho? 
 17 Inenso ndiyankhulapo tsopano; 
nanenso ndinena zimene ndikudziwa. 
 18 Pakuti ndili nawo mawu ambiri, 
ndipo mtima wanga ukundikakamiza; 
 19 mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, 
ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika. 
 20 Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; 
ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha. 
 21 Sindidzakondera munthu wina aliyense, 
kapena kuyankhula zoshashalika, 
 22 pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, 
Mlengi wanga akanandilanga msanga.”