47
Kugwa kwa Babuloni 
 1 “Tsika, ndi kukhala pa fumbi, 
iwe namwali, Babuloni; 
khala pansi wopanda mpando waufumu, 
iwe namwali, Kaldeya 
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera 
kumugwira mosamala. 
 2 Tenga mphero ndipo upere ufa; 
chotsa nsalu yako yophimba nkhope 
kwinya chovala chako mpaka ntchafu 
ndipo woloka mitsinje. 
 3 Maliseche ako adzakhala poyera 
ndipo udzachita manyazi. 
Ndidzabwezera chilango 
ndipo palibe amene adzandiletse.” 
 4 Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, 
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. 
 5 “Khala chete, ndipo lowa mu mdima, 
iwe namwali, Kaldeya; 
chifukwa sadzakutchulanso 
mfumukazi ya maufumu. 
 6 Ndinawakwiyira anthu anga, 
osawasamalanso. 
Ndinawapereka manja mwako, 
ndipo iwe sunawachitire chifundo. 
Iwe unachitira nkhanza 
ngakhale nkhalamba. 
 7 Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse 
ngati mfumukazi.’ 
Koma sunaganizire zinthu izi 
kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere. 
 8 “Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, 
amene ukukhala mosatekesekawe, 
umaganiza mu mtima mwako kuti, 
‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. 
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, 
ndipo ana anga sadzamwalira.’ 
 9 Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, 
zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: 
ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. 
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu 
ngakhale ali ndi amatsenga ambiri 
ndi mawula amphamvu. 
 10 Iwe unkadalira kuyipa kwako 
ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ 
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, 
choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, 
‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’ 
 11 Ngozi yayikulu idzakugwera 
ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. 
Mavuto adzakugwera 
ndipo sudzatha kuwachotsa; 
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa 
chidzakugwera mwadzidzidzi. 
 12 “Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, 
pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, 
wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. 
Mwina udzatha kupambana 
kapena kuopsezera nazo adani ako. 
 13 Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! 
Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. 
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi 
zimene ziti zidzakuchitikire. 
 14 Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; 
adzapsa ndi moto. 
Sangathe kudzipulumutsa okha 
ku mphamvu ya malawi a moto. 
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; 
kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi. 
 15 Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, 
anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito 
ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. 
Onse adzamwazika ndi mantha, 
sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”