42
Mtumiki wa Yehova 
 1 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza, 
amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye. 
Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo, 
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo. 
 2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu, 
kapena mawu ake kumveka mʼmisewu. 
 3 Bango lophwanyika sadzalithyola, 
ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa. 
Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi; 
 4 sadzafowoka kapena kukhumudwa 
mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi, 
ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.” 
 5 Yehova Mulungu 
amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, 
amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, 
amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, 
ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti, 
 6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama; 
ndikugwira dzanja ndipo 
ndidzakuteteza. 
Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu 
ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina. 
 7 Udzatsekula maso a anthu osaona, 
udzamasula anthu a mʼndende 
ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima. 
 8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! 
Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense 
kapena matamando anga kwa mafano. 
 9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi, 
ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano; 
zinthuzo zisanaonekere 
Ine ndakudziwitsani.” 
Nyimbo Yotamanda Yehova 
 10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, 
mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi, 
inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo. 
Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova. 
 11 Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo; 
midzi ya Akedara ikondwere. 
Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe; 
afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri. 
 12 Atamande Yehova 
ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse. 
 13 Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu, 
adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo; 
akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo 
ndipo adzagonjetsa adani ake. 
 14 Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali, 
ndakhala ndili phee osachita kanthu. 
Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira, 
ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu. 
 15 Ndidzawononga mapiri ndi zitunda 
ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse; 
ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba 
ndipo ndidzawumitsa maiwe. 
 16 Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe, 
ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo; 
ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala 
ndipo ndidzasalaza malo osalala. 
Zimenezi ndizo ndidzachite; 
sindidzawataya. 
 17 Koma onse amene amadalira mafano 
amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ 
ndidzawachititsa manyazi kotheratu. 
Aisraeli Alephera Kuphunzira 
 18 “Imvani, agonthi inu; 
yangʼanani osaona inu, kuti muone!  19 Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi? 
Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma? 
Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano, 
kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova? 
 20 Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale; 
makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.” 
 21 Chinamukomera Yehova 
chifukwa cha chilungamo chake, 
kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana. 
 22 Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo, 
onsewa anawakola mʼmaenje 
kapena akuwabisa mʼndende. 
Tsono asanduka chofunkha 
popanda wina wowapulumutsa 
kapena kunena kuti, 
“Abwezeni kwawo.” 
 23 Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi 
kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo? 
 24 Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha, 
ndi Israeli kwa anthu akuba? 
Kodi si Yehova, 
amene ife tamuchimwirayu? 
Pakuti sanathe kutsatira njira zake; 
ndipo sanamvere malangizo ake. 
 25 Motero anawakwiyira kwambiri, 
nawavutitsa ndi nkhondo. 
Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse; 
motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.