35
Chimwemwe cha Opulumutsidwa 
 1 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; 
dziko lowuma lidzakondwa 
ndi kuchita maluwa.  2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka 
lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. 
Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, 
maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. 
Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, 
ukulu wa Mulungu wathu. 
 3 Limbitsani manja ofowoka, 
limbitsani mawondo agwedegwede; 
 4 nenani kwa a mitima yamantha kuti; 
“Limbani mtima, musachite mantha; 
Mulungu wanu akubwera, 
akubwera kudzalipsira; 
ndi kudzabwezera chilango adani anu; 
akubwera kudzakupulumutsani.” 
 5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso 
ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka. 
 6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, 
ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. 
Akasupe adzatumphuka mʼchipululu 
ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma, 
 7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe, 
nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. 
Pamene panali mbuto ya ankhandwe 
padzamera udzu ndi bango. 
 8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; 
ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. 
Anthu odetsedwa 
sadzayendamo mʼmenemo; 
zitsiru sizidzasochera mʼmenemo. 
 9 Kumeneko sikudzakhala mkango, 
ngakhale nyama yolusa sidzafikako; 
sidzapezeka konse kumeneko. 
Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu. 
 10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. 
Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; 
kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. 
Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, 
ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.