28
Tsoka kwa Efereimu 
 1 Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu. 
Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa 
limene lili pa mutu pa anthu 
oledzera a mʼchigwa chachonde. 
 2 Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga. 
Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga, 
ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho; 
ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza. 
 3 Ulamuliro wa atsogoleri oledzera 
a ku Efereimu adzawuthetsa. 
 4 Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa 
lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja, 
udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa 
imene munthu akangoyiona amayithyola 
nthawi yokolola isanakwane. 
 5 Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse 
adzakhala ngati nkhata yaufumu, 
chipewa chokongola 
kwa anthu ake otsala. 
 6 Iye adzapereka mtima 
wachilungamo kwa oweruza, 
adzakhala chilimbikitso kwa 
amene amabweza adani pa zipata za mzinda. 
 7 Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo 
ndipo akusochera chifukwa cha mowa: 
ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa 
ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo; 
akusochera chifukwa cha mowa, 
akudzandira pamene akuona masomphenya, 
kupunthwa pamene akupereka chigamulo. 
 8 Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha 
ndipo palibenso malo wopanda zonyansa. 
 9 Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani? 
Uthengawu akufuna kufotokozera yani? 
Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa, 
kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere? 
 10 Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono 
lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, 
phunziro ndi phunziro. 
Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.” 
 11 Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino. 
Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene 
 12 anakuwuzani kuti, 
“Malo opumulira ndi ano, 
otopa apumule, malo owusira ndi ano.” 
Koma inu simunamvere. 
 13 Choncho Yehova adzakuphunzitsani 
pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, 
mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. 
Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo, 
adzapweteka ndi kukodwa mu msampha 
ndipo adzakutengani ku ukapolo. 
 14 Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova, 
inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu. 
 15 Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa, 
ife tachita mgwirizano ndi manda. 
Pamene mliri woopsa ukadzafika 
sudzatikhudza ife, 
chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu 
ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.” 
 16 Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: 
“Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri 
ngati maziko mu Ziyoni, 
mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; 
munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka. 
 17 Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake, 
ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere; 
matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza, 
ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako. 
 18 Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; 
mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. 
Pakuti mliri woopsa udzafika, 
ndipo udzakugonjetsani. 
 19 Ndipo ukadzangofika udzakutengani. 
Udzafika mmawa uliwonse, 
usiku ndi usana.” 
Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu 
adzaopsedwa kwambiri. 
 20 Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo; 
ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe. 
 21 Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu 
adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni; 
adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo, 
ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa. 
 22 Tsopano lekani kunyoza, 
mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri; 
Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti, 
“Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.” 
 23 Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga; 
mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena. 
 24 Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha? 
Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha? 
 25 Pamene iye wasalaza mundawo, 
kodi samafesa mawere ndi chitowe? 
Kodi suja samadzala tirigu 
ndi barele mʼmizere yake, 
nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo? 
 26 Mulungu wake amamulangiza 
ndi kumuphunzitsa njira yabwino. 
 27 Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero, 
kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta; 
mawere amapuntha ndi ndodo 
ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo. 
 28 Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi, 
komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke. 
Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta, 
koma akavalo ake satekedza tiriguyo. 
 29 Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, 
wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.