21
Za Chilango cha Babuloni 
 1 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. 
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, 
kuchokera ku chipululu, 
dziko lochititsa mantha. 
 2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: 
Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. 
Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! 
Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni. 
 3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, 
ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; 
ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, 
ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona. 
 4 Mtima wanga ukugunda, 
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha; 
chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna 
chasanduka chinthu choopsa kwa ine. 
 5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, 
akuyala mphasa, 
akudya komanso kumwa! 
Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, 
pakani mafuta zishango zanu!” 
 6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi; 
“Pita, kayike mlonda 
kuti azinena zimene akuziona. 
 7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo 
ndipo akuyenda awiriawiri, 
okwera pa bulu 
kapena okwera pa ngamira, 
mlondayo akhale tcheru kwambiri.” 
 8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti, 
“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera; 
Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera. 
 9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta 
ali ndi gulu la akavalo. 
Mmodzi wa iwo akuti, 
‘Babuloni wagwa, wagwa! 
Mafano onse a milungu yake 
agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ” 
 10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu, 
ine ndikukuwuzani zimene ndamva 
ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, 
Mulungu wa Israeli. 
Za Chilango cha Edomu 
 11 Uthenga wonena za Duma: 
Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, 
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti? 
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?” 
 12 Mlonda akuyankha kuti, 
“Kukucha, koma kudanso. 
Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; 
ndipo ubwerenso udzafunse.” 
Za Chilango cha Arabiya 
 13 Uthenga wonena za Arabiya: 
Inu anthu amalonda a ku Dedani, 
amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya, 
 14 perekani madzi kwa anthu aludzu. 
Inu anthu a ku Tema 
perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo. 
 15 Iwo akuthawa malupanga, 
lupanga losololedwa, 
akuthawa uta wokokakoka 
ndiponso nkhondo yoopsa. 
 16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu.  17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.