17
Uthenga Wotsutsa Damasiko 
 1 Uthenga wonena za Damasiko: 
“Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda, 
koma udzasanduka bwinja. 
 2 Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu 
ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi 
popanda wina woziopseza. 
 3 Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, 
ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; 
Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu 
monga anthu a ku Israeli,” 
akutero Yehova Wamphamvuzonse. 
 4 “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira; 
ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi. 
 5 Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu 
umene anatsiriza kukolola. 
Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu 
anthu atatha kukunkha ngala za tirigu. 
 6 Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale 
monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni 
kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi 
mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” 
akutero Yehova, Mulungu wa Israeli. 
 7 Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo 
ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli. 
 8 Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe, 
ntchito ya manja awo, 
ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera, 
ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga. 
 9 Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja. 
 10 Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu; 
simunakumbukire Thanthwe, linga lanu. 
Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino, 
ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa, 
 11 nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo 
ndi kuphukira maluwa mmawa mwake, 
komabe zimenezi sizidzakupindulirani 
pa tsiku la mavuto. 
 12 Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri, 
akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja! 
Aa, phokoso la anthu a mitundu ina, 
akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu! 
 13 Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri, 
koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula. 
Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri, 
ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe. 
 14 Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika, 
ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa. 
Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu, 
gawo la amene amatibera zinthu zathu.