15
Za Kulangidwa kwa Mowabu 
 1 Uthenga wonena za Mowabu: 
Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa, 
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. 
Mzinda wa Kiri wawonongedwa, 
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. 
 2 Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, 
akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; 
anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. 
Mutu uliwonse wametedwa mpala, 
ndipo ndevu zonse zametedwa. 
 3 Mʼmisewu akuvala ziguduli; 
pa madenga ndi mʼmabwalo 
aliyense akulira mofuwula, 
misozi ili pupupu. 
 4 Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula, 
mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi. 
Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula, 
ndipo ataya mtima. 
 5 Inenso ndikulirira Mowabu; 
chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari 
ndi Egilati-Selisiya 
akupita akulira ku chikweza cha Luhiti, 
Akulira mosweka mtima 
pa njira yopita ku Horonaimu; 
akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo. 
 6 Madzi a ku Nimurimu aphwa 
ndipo udzu wauma; 
zomera zawonongeka 
ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala. 
 7 Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga, 
achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi. 
 8 Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu; 
kulira kwawo kosweka mtima kukumveka 
mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu. 
 9 Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi, 
komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni, 
mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu 
ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.