12
Nyimbo za Mayamiko 
 1 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati: 
“Ndikukuyamikani, Inu Yehova; 
chifukwa ngakhale munandipsera mtima, 
mkwiyo wanu wachoka, 
ndipo mwanditonthoza. 
 2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga; 
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha. 
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; 
Iye wakhala chipulumutso changa.” 
 3 Mudzakondwera popeza Yehova 
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu. 
 4 Tsiku limenelo mudzati: 
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake; 
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, 
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. 
 5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu; 
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi. 
 6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; 
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”